13 cifukwa ali wolipidwa, ndipo sasamala nkhosa.
14 Ine ndine Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira ine,
15 monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga cifukwa ca nkhosa.
16 Ndipo nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi,
17 Cifukwa ca ici Atate andikonda Ine, cifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso,
18 Palibe wina andicotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndiri nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndiri nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa. Atate wanga.
19 Panakhalanso kutsutsana pakati pa Ayuda cifukwa ca mau awa.