17 Cifukwa ca ici Atate andikonda Ine, cifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso,
18 Palibe wina andicotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndiri nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndiri nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa. Atate wanga.
19 Panakhalanso kutsutsana pakati pa Ayuda cifukwa ca mau awa.
20 Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi ciwanda, nacita misala; mukumva iye bwanji?
21 Ena ananena, Mau awa sali a munthu wogwidwa ciwanda. Kodi ciwanda cikhoza kumtsegulira maso wosaona?
22 Koma kunali phwando la kukonzersanso m'Yerusalemu; nyengoyo ndi yacisanu.
23 Ndipo Yesu analikuyendayenda m'Kacisi m'khumbi la Solomo,