3 Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mau ace; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina ao, nazitsogolera kunja.
4 Pamene adaturutsa zonse za iye yekha, azitsogolera; ndi nkhosa zimtsata iye; cifukwa zidziwa mau ace.
5 Koma mlendo sizidzamtsata, koma zidzamthawa; cifukwasizidziwa mau a alendo.
6 Fanizo ili Yesu ananena kwa iwo; koma sanazindikira zimene Yesu analikulankhula nao.
7 Cifukwa cace Yesuananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa.
8 Onse amene anadza m'tsogolo mwa Ine ali akuba, ndi olanda: koma nkhosa sizinamva iwo.
9 Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulu-mutsidwa, nadzalowa, nadzaturuka, nadzapeza busa.