16 Izisanazidziwa aku phunzira ace poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukila kuti izi zinalembedwa za iye, ndi kuti adamcitira iye izi.
17 Pamenepo khamulo limene linali pamodzi ndi iye, m'mene anaitana Lazaro kuturuka kumanda, namuukitsa kwa akufa, anacita umboni.
18 Cifukwa ca icinso khamulo linadza kudzakomana ndi iye, cifukwa anamva kuti iye adacita cizindikilo ici.
19 Cifukwa cace Afarisi ananena wina ndi mnzace, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pace pa iye.
20 Koma panali Ahelene ena mwa iwo akukwera kunka kukalambira paphwando,
21 Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa m'Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu.
22 Filipo anadza nanena kwa Andreya; nadza Andreya ndi Filipo, nanena ndi Yesu.