2 Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adathakuika mu mtima wace wa Yudase mwana wa Simoni Isikariote, kuti akampereke iye,
3 Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa iye zonse m'manja mwace, ndi kuti anacokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu,
4 ananyamuka pamgonero, nabvula malaya ace; ndipo m'mene adatenga copukutira, anadzimanga m'cuuno.
5 Pomwepo anathira madzi m'nsambidwe, nayamba kusambitsa mapazi a akuphunzira ace, ndi kuwapukuta ndi copukutira, cimene anadzimanga naco,
6 Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi iye, Ambuye, kodi Inu mundisambitsa ine mapazi?
7 Yesu anayankha nati kwa iye, Cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwace.
8 Petro ananena ndi iye, Simudzasambitsa mapazi anga ku nthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe colandira pamodzi ndi Ine.