8 Petro ananena ndi iye, Simudzasambitsa mapazi anga ku nthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe colandira pamodzi ndi Ine.
9 Simoni Petro ananena ndi iye, Ambuye, si mapazi anga okha, komanse manja ndi mutu.
10 Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.
11 Pakuti anadziwa amene adzampereka iye; cifukwa ca ici anati, Simuli oyera nonse.
12 Pamenepo, atatha iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ace, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga cimene ndakucitirani inu; mucizindikira kodi?
13 Inu mundicha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene.
14 Cifukwa cace, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzaceo