19 Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.
20 Tsiku lo mwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu.
21 Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo line ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsandekha kwa iye.
22 Yudase, si Isikariote, ananena ndi iye, Ambuye, cacitika ciani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi?
23 Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.
24 Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo 1 mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine.
25 Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu.