4 Pamenepo Yesu, podziwa zonse zirinkudza pa iye, anaturuka, nati kwa iwo, Mufuna yani?
5 Anayankha iye, Yesu Mnazarayo. Yesu ananena nao, Ndine. Koma Yudase yemwe, wompereka iye, anaima nao pamodzi.
6 Ndipo m'mene anati kwa iwo, Ndine, anabwerera m'mbuyo, nagwa pansi.
7 Pamenepo anawafunsanso, Mufuna yani? koma iwo anati, Yesu Mnazarayo.
8 Yesu anayankha, Ndati, Ndine; cifukwa cace ngati mufuna Ine, lekani awa amuke;
9 kuti akwaniridwe mau amene ati, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindinataya mmodzi.
10 Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, analisolola nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namsenga khutu lace lamanja. Koma dzina lace la kapoloyo ndiye Malko.