1 Pamenepo tsono Pilato anatenga Yesu, namkwapula.
2 Ndipo asilikari, m'mene analuka korona waminga anambveka pamutu pace, nampfunda iye maraya acibakuwa;
3 nadza kwa iye, nanena, Tikuoneni, Mfumu ya Ayuda! nampanda khofu.
4 Ndipo Pilato anaturukanso kunja, nanena nao, Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa iye cifukwa ciri conse.
5 Pamenepo Yesu anaturuka kunja, atabvala korona waminga; ndi maraya acibakuwa, Ndipo ananena nao, Taonani munthuyu!