1 Ndipo tsiku lacitatu pariali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo amace wa Yesu anali komweko.
2 Ndipo Yesu yemwe ndi akuphunzira ace anaitanidwa ku ukwatiwo.
3 Ndipo pakutha vinyo, amace wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo,
4 Yesu nanena naye, Mkazi, ndiri ndi ciani ndi inu? nthawi yanga siinafike.
5 Amace ananena kwa atumiki, Cimene ciri conse akanena kwa inu, citani.
6 Ndipopanali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.
7 Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, nde nde nde.