24 Koma Tomasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, wochedwa Didimo, sanakhala nao pamodzi, pamene Yesu anadza.
25 Cifukwa cace akuphunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ace cizindikilo ca misomaliyo, ndi kuika cala canga m'cizindikilo ca misomaliyo, ndi kuika dzanja langa ku nthiti yace; sindidzakhulupira.
26 Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu akuphunzira ace analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao: Yesu anadza, makomo ali citsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu.
27 Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera naco cala cako kuno, nuone manja anga; ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike ku nthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupira, koma wokhulupira.
28 Tomasi anayankha nati kwa iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.
29 Yesu ananena kwa iye, Cifukwa wandiona Ine, wakhulupira; odala iwo akukhulupira, angakhale sanaona.
30 Ndipo zizindikilo zina zambiri Yesu anazicita pamaso pa akuphunzira ace, zimene sizinalembedwa m'buku ili;