27 Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera naco cala cako kuno, nuone manja anga; ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike ku nthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupira, koma wokhulupira.
28 Tomasi anayankha nati kwa iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.
29 Yesu ananena kwa iye, Cifukwa wandiona Ine, wakhulupira; odala iwo akukhulupira, angakhale sanaona.
30 Ndipo zizindikilo zina zambiri Yesu anazicita pamaso pa akuphunzira ace, zimene sizinalembedwa m'buku ili;
31 koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Kristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupira mukhale nao moyo m'dzina lace.