34 Yesu ananena nao, Cakudya canga ndico kuti ndicite cifuniro ca iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza nchito yace.
35 Kodi simunena inu, kuti, Yatsala miyezi inai, ndipo kudza kumweta? Onani ndinena kwa inu, Kwezani maso anu, nimuyang'ane m'minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta.
36 Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira cobala ku moyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo.
37 Pakuti m'menemo conenaco ciri coona, Wofesa ndi wina, womweta ndi winanso.
38 Ine ndinatuma inu kukamweta cimene simunagwirirapo nchito: ena anagwira nchito, ndipo inu mwalowa nchito yao.
39 Ndipo m'mudzi mula anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira iye cifukwa ca mau a mkazi, wocita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu ziri zonse ndinazicita.
40 Cifukwa cace pamene Asamariya anadza kwa iye, anamfunsa akhale nao; ndipo anakhala komweko masiku awiri.