34 Ndipo Ine sindilandira umboni kwa munthu: koma ndinena izi, kuti inu mukapulumutsidwe.
35 Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwace kanthawi.
36 Koma Ine ndiri nao umboni woposa wa Yohane; pakuti nchito zimene Atateanandipatsa ndizitsirize, nchito zomwezo ndizicita zindicitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.
37 Ndipo Atate wonditumayo, 1 Iyeyu wandicitira Ine umboni. Simunamva mau ace konse, kapena maonekedwe ace simunaona.
38 Ndipo mulibe mau ace okhala mwa inu; cifukwa kuti amene Iyeyu anatuma, inu simumkhulupirira ameneyo.
39 2 Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundicitira Ine umboni ndi iwo omwewo;
40 ndipo 3 simufuna kudza kwa Ine, kuti mukhale nao moyo.