28 Pamenepo anati kwa iye, Ticite ciani, kuti ticite nchito za Mulungu?
29 Yesu anayankha nati kwa iwo, Nchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire iye amene Iyeyo anamtuma.
30 Cifukwa cace anati kwa iye, Ndipo mucita cizindikilo canji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? mucita ciani?
31 Atate athu anadya mana m'cipululu; monga kwalembedwa, Mkate wocokera m'mwamba anawapatsa iwo kudya,
32 Cifukwa cace Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba.
33 Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kucokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.
34 Pamenepo anati kwa iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umene nthawi zonse.