1 Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda m'Galileya; pakuti sanafuna kuyendayenda m'Yudeya, cifukwa Ayuda anafuna kumupha iye.
2 Koma phwando la Ayuda, phwando la misasa, linayandikira.
3 Cifukwa cace abale ace anati kwa iye, Cokani pano, mumuke ku Yudeya, kuti akuphunzita anunso akapenye nchito zanu zimenemucita.
4 Pakuti palibe munthu acita kanthu mobisika, nafuna yekha kukhala poyera, Ngati mucita izi, dzionetsereni eni nokha kwa dziko lapansi,
5 Pakuti angakhale abale ace sanakhulupirira iye.