30 Pamenepo anafuna kumgwira iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, cifukwa nthawi yace siinafike.
31 Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira iye; ndipo ananena, Pamene Kristu akadza kodi adzacita zizindikilo zambiri zoposa zimene adazicita ameneyo?
32 Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za iye; ndipo ansembe akulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire iye.
33 Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndiri ndi inu, ndipo ndimuka kwa iye wondituma Ine.
34 Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndiri Ine, inu simungathe kudzapo.
35 Cifukwa cace Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza iye? kodi adzamuka kwa Ahelene obalalikawo, ndi kuphunzitsa Ahelene?
36 Mau awa amene ananena ndi ciani, Mudzandifunafuna osandipeza Ine: ndipo pomwe ndiri Ine, inu simungathe kudzapo?