1 Koma Yesu anamuka ku phiri la Azitona.
2 Komac mamawa anadzanso kuKacisi, ndipo anthu onse anadza kwa iye; ndipo m'mene anakhala pansi anawaphunzitsa.
3 Koma alembi ndi Afarisi anabwera naye kwa iye mkazi wogwidwa m'cigololo, ndipo pamene anamuimika iye pakati,
4 ananena kwa iye, Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa alimkucita cigololo.
5 Koma m'cilamulo Mose anatilamulira, ttwaponye miyala otere. Cifukwa cace Inu munena ciani za iye?
6 Koma ici ananena kuti amuyese iye, kuti akhale naco comneneza iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi cala cace.