45 Koma Ine, cifukwa ndinena coonadi, simukhulupirira Ine.
46 Ndani mwa inu anditsutsa Ine za cimo? Ngati ndinena coonadi, simundikhulupirira Ine cifukwa ninji?
47 6 Iye wocokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva cifukwa cakuti simuli a kwa Mulungu,
48 Ayuda anayankha nati kwa iye, Kodi sitinenetsa kun Inu ndinu Msamariya, ndipo 7 muli ndi ciwanda?
49 Yesu anayankha, Ndiribe ciwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.
50 Koma 8 Ine sinditsata ulemerero wanga; alipo woutsata ndi wakuweruza.
51 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, 9 Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse.