15 Davide naitana wina wa anyamatawo, nati, Sendera numkanthe, Ndipo anamkantha, nafa iye.
16 Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; cifukwa pakamwa pako padacita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova.
17 Ndipo Davide analirira Sauli ndi Jonatani mwana wace ndi nyimbo iyi ya maliro;
18 nawauza aphunzitse ana Ayuda nyimbo iyi ya Uta, onani inalembedwa m'buku la Jasari:-
19 Ulemerero wako, Israyeli, unaphedwa pa misanje yako.Ha! adagwa amphamvu
20 Usacinene ku Gati,Usacibukitse m'makwalala a Asikeloni,Kuti ana akazi a Afilisti angasekere,Kuti ana akazi a osadulidwawo angapfuule mokondwera.
21 Mapiri inu a Giliboa,Pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka.Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa,Cikopa ca Sauli, monga ca wosadzozedwa ndi mafuta.