2 pa tsiku lacitatu, onani, munthu anaturuka ku zithando za Sauli, ali ndi zobvala zace zong'ambika, ndi dothi pamutu pace; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.
3 Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israyeti.
4 Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Sauli ndi Jonatani mwana wace anafanso.
5 Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwang kuti Sauli ndi Jonatani mwana wace anafa?
6 Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda pa phiri la Giliboa, ndinaona, Sauli alikuyedzamira nthungo yace, ndi magareta ndi apakavalo anamyandikiza.
7 Ndipo iye pakuceukira m'mbuyo mwace anandiona, nanditana. Ndipo ndinayankha, Ndine.
8 Nanena, Ndiwe yani? Ndipo ndinayankha kuti, Ndine M-amaleki.