3 Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israyeti.
4 Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Sauli ndi Jonatani mwana wace anafanso.
5 Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwang kuti Sauli ndi Jonatani mwana wace anafa?
6 Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda pa phiri la Giliboa, ndinaona, Sauli alikuyedzamira nthungo yace, ndi magareta ndi apakavalo anamyandikiza.
7 Ndipo iye pakuceukira m'mbuyo mwace anandiona, nanditana. Ndipo ndinayankha, Ndine.
8 Nanena, Ndiwe yani? Ndipo ndinayankha kuti, Ndine M-amaleki.
9 Ndipo anati kwa ine, Uime pa ine nundiphe, cifukwa kuwawa mtima kwandigwera ine, popeza ndikali moyobe.