1 Ndipo kunali pofikanso caka, nyengo yakuturuka mafumu, Davide anatumiza Yoabu, pamodzi ndi anyamata ace, ndi Aisrayeli onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsaliraku Yerusalemu.
2 Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wace nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wocititsa kaso pomuyang'ana.
3 Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu mkazi wa Uriya Mhiti?
4 Ndipo bavide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adacoka mumsambo; ndipo anabwereranso ku nyumba yace.
5 Ndipo mkaziyo anaima, natumiza munthu nauza Davide, kuti, Ndiri ndi pakati.
6 Davide natumiza kwa Yoabu, nati, Unditumizire Uriya Mhiti. Ndipo Yoabu anatumiza Uriya kwa Davide.
7 Ndipo pakufika kwa iye Uriya uja, Davide anamfunsa kuti, Yoabu ali bwanji? ndi anthu ali bwanji? ndi nkhondo iri bwanji?