14 Ndipo m'mawa Davide analembera Yoabu kalata, wopita nave Uriya.
15 Ndi m'kalatamo analemba kuti, Mumuike Uriya pa msongwe wa nkhondo yolimba, ndipo mumlekerere kuti akanthidwe nafe.
16 Ndipo Yoabu atayang'anira mudziwo, anaika Uriye pomwe anadziwa kuti pali ngwazi.
17 Ndipo akumudziwo anaturuka, namenyana ndi Yoabu; ndipo adagwapo anthu ena, ndiwo a anyamata a Davide; ndi Uriya Mhiti anafanso.
18 Pamenepo Yoabu anatumiza munthu nauza Davide zonse za nkhondoyi;
19 nauza mthengawo kuti, Utatsiriza kuuza mfumu zonse za nkhondozo;
20 kudzali kuti ukapsa mtima wa mfumu nikati kwa iwe, Cifukwa ninji munayandikira pafupi potere pamudzi kukamenyana nao? Simunadziwa kodi kuti apalingawo adzaponya?