11 Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzacotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa liri denene.
12 Pakuti iwe unacicita m'tseri; koma Ine ndidzacita cinthu ici pamaso pa Aisrayeli onse, dzuwa liri nde.
13 Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinacimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wacotsa chimo lanu, simudzafa.
14 Koma popeza pakucita ici munapatsa cifukwa cacikuru kwa adani a Yehova ca kucitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.
15 Ndipo Natani anamuka kwao. Ndipo Yehova anadwaza mwana amene mkazi wa Uriya anambalira Davide, nadwala kwambiri.
16 Cifukwa cace Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi.
17 Ndipo akuru a m'nyumba yace ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.