15 Ndipo Natani anamuka kwao. Ndipo Yehova anadwaza mwana amene mkazi wa Uriya anambalira Davide, nadwala kwambiri.
16 Cifukwa cace Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi.
17 Ndipo akuru a m'nyumba yace ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.
18 Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwang kuti mwana wafa; sadzadzicitira coipa nanga?
19 Koma pamene Davide anaona anyamata ace alikunong'onezana, Davide anazindikira kuti mwanayo adafa; Davide nanena ndi anyamata ace, Kodi mwanayo wafa? Nati iwo, Wafa.
20 Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zobvala; nafika ku nyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika ku nyumba yace; ndipo powauza anamuikira cakudya, nadya iye.
21 Pamenepo anyamata ace ananena naye, Ici mwacita nciani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya,