12 Inu ndinu abale anga, muli pfupa langa ndi mnofu wanga; cifukwa ninji tsono muli am'mbuyo koposa onse kubwera nayo mfumu?
13 Ndipo munene ndi Amasa, Suli pfupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala cikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yoabu.
14 Ndipo iye anakopa mitima ya anthu onse a Yuda, monga munthu mmodzi, natumiza iwo kwa mfumu, nati, Mubwere inu ndi anyamata anu onse.
15 Comweco mfumu inabwera nifika ku Yordano. Ndipo Ayuda anadza ku Giligala, kuti akakomane ndi mfumu, ndi kumuolotsa mfumu pa Yordano.
16 Ndipo Simeyi, mwana wa Gera, Mbenjammi, wa ku Bahurimu, anafulumira natsika pamodzi ndi anthu a Yuda kuti akakomane ndi mfumu Davide.
17 Ndipo anali nao anthu cikwi cimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saul; ndi ana ace amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ace makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordano pamaso pa mfumu.
18 Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kucita comkomera. Ndipo Simeyi mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordano.