3 Ndipo Davide anakwera nao anyamata ace okhala naye, munthu yense ndi banja lace; iwowa nakhala m'midzi ya Hebroni.
4 Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda.Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Jabezi Gileadi ndiwo amene anamuika Sauli.
5 Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Jabezi Gileadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munacitira cokoma ici mbuye wanu Sauli, ndi kumuika.
6 Ndipo tsopano Yehova acitire inu cokoma ndi coonadi; inenso ndidzakubwezerani cokoma ici, popeza munacita cinthuci.
7 Cifukwa cace tsono manja anu alimbike, nimucite camuna; pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao.
8 Koma Abineri, mwana wa Neri, kazembe wa khamu la ankhondo a Sauli anatenga Isiboseti mwana wa Sauli, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
9 namlonga ufumu wa pa Gileadi ndi Aasuri ndi Jezreeli ndi Efraimu ndi Benjamini ndi Aisrayeli onse.