4 Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda.Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Jabezi Gileadi ndiwo amene anamuika Sauli.
5 Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Jabezi Gileadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munacitira cokoma ici mbuye wanu Sauli, ndi kumuika.
6 Ndipo tsopano Yehova acitire inu cokoma ndi coonadi; inenso ndidzakubwezerani cokoma ici, popeza munacita cinthuci.
7 Cifukwa cace tsono manja anu alimbike, nimucite camuna; pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao.
8 Koma Abineri, mwana wa Neri, kazembe wa khamu la ankhondo a Sauli anatenga Isiboseti mwana wa Sauli, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
9 namlonga ufumu wa pa Gileadi ndi Aasuri ndi Jezreeli ndi Efraimu ndi Benjamini ndi Aisrayeli onse.
10 Ndipo Isiboseti mwana wa Sauli anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israyeli, nacita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide.