5 Pakuti mafunde a imfa anandizinga,Mitsinje ya zopanda pace inandiopsa ine.
6 Zingwe za kumanda zinandizingira;Misampha ya imfa inandifikira ine.
7 M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova,Inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga;Ndipo Iye anamva mau anga ali m'kacisi wace,Ndi kulira kwanga kunafika ku makutuace.
8 Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira.Maziko a dziko la kumwamba anasunthikaNagwedezeka, cifukwa iye anakwiya.
9 M'mphuno mwace munaturuka utsi,Ndi moto woturuka m'kamwa mwace unaononga;Makala anayaka nao.
10 Anaweramitsa miyambanso, natsika;Ndipo mdima wandiwe-yani unali pansi pa mapazi ace.
11 Ndipo iye anaberekeka pa Kerubi nauluka;Inde anaoneka pa mapiko a mphepo,