27 Pofikanso Abineri ku Hebroni, Yoabu anampambutsa kupita nave pakati pa cipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, cifukwa ca mwazi wa Asaheli mbale wace.
28 Ndipo pambuyo pace, pakucimva Davide, anati, Ine ndi ufumu wanga tikhala osacimwira mwazi wa Abineri mwana wa Neri, nthawi zonse, pamaso pa Yehova;
29 cilango cigwere pa mutu wa Yoabu ndi pa nyumba yonse ya atate wace; ndipo kusasoweke ku nyumba ya Yoabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa cakudya.
30 Motero Yoabu ndi Abisai mbale wace adapha Abineri, popeza iye adapha mbale wao Asaheli ku Gibeoni, kunkhondo.
31 Ndipo Davide anati kwa Yoabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng'ambani zobvala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m'cuuno, nimulire Abineri. Ndipo mfumu Davide anatsata cithatha.
32 Ndipo anaika Abineri ku Hebroni; ndi mfumu inakweza mau ace nilira ku manda a Abineri, nalira anthu onse.
33 Ndipo mfumu inanenera Abineri nyimbo iyi ya maliro, niti,Kodi Abineri anayenera kufa ngati citsiru?