2 Samueli 4:4 BL92

4 Ndipo Jonatani mwana wa Sauli, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi, Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Sauli ndi Jonatani yocokera ku Jezreeli; ndipo mlezi wace adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lace ndiye Mefiboseti.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 4

Onani 2 Samueli 4:4 nkhani