1 Ndipo pamene Isiboseti mwana wa Sauli, anamva kuti Abineri adakafera ku Hebroni, manja ace anafoka, ndi Aisrayeli onse anabvutika.
2 Ndipo Isiboseti, mwana wa Sauli anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lace Baana, ndi dzina la mnzace ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini;
3 ndi Abeeroti anathawira ku Gitaimu; kumeneko amakhalira kufikira lero lino.
4 Ndipo Jonatani mwana wa Sauli, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi, Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Sauli ndi Jonatani yocokera ku Jezreeli; ndipo mlezi wace adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lace ndiye Mefiboseti.
5 Ndipo Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti, anamuka, nafika ku nyumba ya Isiboseti potentha dzuwa popumula iye usana.
6 Ndipo iwo analowanso kufikira m'kati mwa nyumba, monga ngati anadzatenga tirigu; namgwaza m'mimba mwace; ndi Rekabu ndi Baana mbale wace anathawa.
7 Koma polowa iwo m'nyumbamo iye ali cigonere pakama pace m'cipindamo, anamkantha, namupha namdula mutu wace, nautenga namuka njira ya kucidikha usiku wonse,