5 Kauze mtumiki wanga Davide, kuti, Atero Yehova, Kodi iwe udzandimangira nyumba yakuti ndikhalemo Ine?
6 pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinaturutsa ana a Israyeli ku Aigupto kufikira lero lomwe, kama ndinayenda m'cihema ndi m'nyumba wamba.
7 M'malo monse ndinayendamo limodzi ndi ana onse a Israyeli kodi ndinanena ndi pfuko limodzi la Aisrayeli, limene ndinalamulira kudyetsa anthu anga Aisrayeli, kuti, Munalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza?
8 Cifukwa cace tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakucotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israyeli,
9 Ndipo ndinali nawe kuli konse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akuru ali pa dziko lapansi,
10 Ndipo ndidzaikira anthu anga Israyeli malo, ndi kuwaoka kuti akakhale m'malo ao a iwo okha, osasunthikanso. Ndipo anthu a mphulupulu sadzawabvutanso, monga poyamba paja,
11 monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israyeli; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.