1 Ndipo Davide anati, Kodi atsalako wina wa nyumba ya Sauli, kuti ndimcitire cifundo cifukwa ca Jonatani?
2 Ndipo panali mnyamata wa m'nyumba ya Sauli dzina lace Ziba; ndipo anamuitana iye afike kwa Davide; ndi mfumuyo inanena naye, Iwe ndiwe Ziba kodi? Nati iye, Ndine mnyamata wanu ame.
3 Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Sauli kuti ndimuonetsere cifundo ca Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Jonatani wopunduka mapazi ace.
4 Ndipo mfumu inanena naye, Ali kuti iyeyo? Ziba nanena kwa mfumu, Onani ali m'nyumba ya Makiri, mwana vya Amiyeli ku Lodebara.