10 Ndipo uzimlimira munda wace, iwe ndi ana ako ndi anyamata ako; nuzibwera nazo zipatso zace kuti mwana wa mbuye wako akhale ndi zakudya; koma Mefiboseti, mwana wa mbuye wako, adzadya pa gome langa masiku onse. Ndipo Ziba anali nao ana amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata makumi awiri.
11 Pomwepo Ziba anati kwa mfumu, Monga mwa zonse mfumu mbuye wanga mulamulira mnyamata wanu, momwemo adzacita mnyamata wanu. Tsono Mefiboseti, anadya pa gome la Davide monga wina wa ana a mfumu.
12 Ndipo Mefiboseti anali ndi mwana wamwamuna wamng'ono, dzina lace ndiye Mika. Ndipo onse akukhala m'nyumba ya Ziba anali anyamata a Mefiboseti.
13 Comweco Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ace onse awiri.