1 Atafa Abimeleki, anauka kupulumutsa Israyeli Tola mwana wa Puwa, mwana wa Dodo munthu wa Isakara; nakhala iye m'Sanriri ku mapiri a Efraimu.
2 Ndipo anaweruza Israyeli zaka makumi awiri ndi zitatu, nafa, naikidwa m'Samiri.
3 Atafa iye, anauka Yairi Mgileadi, naweruza Israyeli zaka makumi awiri mphambu ziwiri.
4 Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu okwera pa ana a aburu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo midzi makumi atatu, ochedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Gileadi.
5 Nafa Yairi, naikidwa m'Kamoni.