Oweruza 7 BL92

Gideoni apitikitsa nkhondo ya Amidyani

1 Pamenepo Yerubaala, ndiye Gideoni, ndi anthu onse okhala naye anauka mamawa, namanga misasa pa citsime ca Harodi, ndi misasa ya Midyani inali kumpoto kwao, pa phiri la More m'cigwa.

2 Ndipo Yehova anati kwa Gideoni. Anthu ali ndi iwe andicurukira kuti ndipereke Midyani m'dzanja lao; angadzitame Israyeli pa Ine, ndi kuti, Dzanja la ine mwini landipulumutsa.

3 Ndipo tsopano, kalalike m'makutu a anthu, ndi kuti, Ali yense wocita mantha, nanjenjemera, abwerere nacoke pa phiri la Gileadi. Ndipo anabwererako anthu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, natsalako zikwi khumi.

4 Ndipo Yehova ananena ndi Gideoni, Anthu akali ocuruka; tsikira nao kumadzi, ndipo ndidzakuyesera iwo komweko; ndipo kudzali kuti iye amene ndimnena kwa iwe, Uyo azimuka nawe, yemweyo azimuka nawe; koma ali yense ndimnena kwa iwe, Uyo asamuke nawe, yemweyo asamuke.

5 Ndipo anatsikira nao anthu kumadzi; ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ali yense akapiza madzi pa lilime lace, monga akhatira garu, ameneyo amuike pa yekha; momwemo ali yense agwada pakumwa.

6 Ndi kuwerenga kwa iwo akukhatira, ndi kuika dzanja lao kukamwa kwao, ndiko mazana atatu; koma ena onse anagwada pakumwa madzi.

7 Ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ndi anthu mazana atatu akukhatira ndidzakupulumutsani, ndi kupereka Amidyani m'dzanja lako; koma amuke anthu awa onse, yense kumalo kwace.

8 Pamenepo anthu anatenga kamba m'dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israyeli amuke, yense kuhema kwace; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midyani inali kunsi kwace m'cigwa.

9 Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m'dzanja lako.

10 Koma ngati uopa kutsika, utsike naye Pura mnyamata wako kumisasa;

11 nudzamva zonena iwo; utatero manja ako adzalimbikitsidwa kutsikira kumisasa. Pamenepo anatsikira ndi Pura mnyamata wace ku cilekezero ca anthu azidaa m'misasa.

12 Ndipo Amidyani ndi Aamaleki ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'cigwa, kucuruka kwao ngati dzombe; ndi ngamila zao zosawerengeka, kucuruka kwao ngati mcenga wa m'mphepete mwa nyanja.

13 Ndipo pakufikako Gideoni, taonani, panali munthu analikufotokozera mnzace loto, nati, Taona, kulota ndinalota, ndipo tapenya, mtanda wa mkate wabarele unakunkhulira-kunkhulira m'misasa ya Midyani, nufika kuhema, numgunda nagwa, numpidigula kuti hema anakhala cigwere.

14 Ndipo mnzace anayankha nati, Ici si cina konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yoasi, munthu wa Israyeli; Mulungu wapereka Midyani ndi a m'misasa onse m'dzanja lace.

15 Ndipo kunali, pakumva Gideoni kufotokozera kwa lotolo ndi tanthauzo lace, anadziwerama; nabwera ku misasa ya Israyeli nati, Taukani, pakuti Yehova wapereka a m'misasa a Midyani m'dzanja lanu.

16 Ndipo anagawa amuna mazana atatu akhale magulu atatu, napatsa malipenga m'manja a iwo onse, ndi mbiya zopanda kanthu, ndi miuni m'kati mwa mbiyazo,

17 Ndipo ananena nao, Mundipenyerere ine, ndi kucita momwemo; ndipo taonani, pakufika ine pa cilekezero ca misasa, kudzali, monga ndicita ine, momwemo muzicita inu.

18 Pamene ndiomba lipenga, ine ndi onse okhala nane, inunso muziomba lipenga pozungulira ponse pa misasa, ndi kunena kuti, Yehova ndi Gideoni.

19 Motero Gideoni ndi amuna zana anali naye anafikira ku cilekezero ca misasa poyambira ulonda wa pakati, atasintha alonda tsopano apa; ndipo anaomba malipenga, naphwanya mbiya zokhala m'manja mwao.

20 Ndi magulu atatuwo anaomba malipenga, naswa mbiyazo, nagwira miuni ndi dzanja lao lamanzere, ndi malipenga m'dzanja lao lamanja kuwaomba; ndipo anapfuula, Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.

21 Ndipo anaima yense m'mbuto mwace pozungulira misasa; pamenepo anathamanga a m'misasa onse, napfuula, nathawa.

22 Ndipo mazana atatuwa anaomba malipenga, ndipo Yehova anakanthanitsa yense mnzace ndi lupanga m'misasa monse; ndi a m'misasa anathawa mpaka ku Betesita ku Zerera, mpaka ku malire a Abelemehola pa Tabati.

23 Pamenepo anthu a Israyeli analalikidwa kucokera ku Nafitali, ndi ku Aseri, ndi ku Manase yense, nalondola Amidyani.

24 Gideoni anatumanso mithenga ku mapiri onse a Efraimu ndi kuti, Tsikani, kukomana ndi Amidyani ndi kutsekereza madooko asanafike iwowa, mpaka ku Beti-bara ndi Yordano. Potero amuna onse a Efraimu anasonkhana pamodzi natsekereza madooko mpaka ku Betibara, ndi Yordano.

25 Ndipo anagwira akalonga awiri a Midyani, Orebi ndi Zeebi; namupha Orebi ku thanthwe la Orebi; ndi Zeebi anamupha ku coponderamo mphesa ca Zeebi, nalondola Amidyani; ndipo anadza nayo mitu ya Orebi ndi Zeebi kwa Gideoni tsidya lija la Yordano.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21