Oweruza 14 BL92

Ukwati wa Samsoni

1 Ndipo Samsoni anatsikira ku Timna, naona mkazi wa ku Timna wa ana akazi a Afilisti.

2 Nakwera iye, nauzaatatewacendi amai wace, nati, Ndapenya mkazi m'Timna wa ana akazi a Afilisti; ndipo tsono munditengere uyu akhale mkazi wanga.

3 Koma atate wace ndi amai wace ananena naye, Kodi palibe mkazi mwa ana akazi a abale ako, kapena mwa anthu a mtundu wanga onse, kuti wamuka kutenga mkazi wa Afilisti osadulidwawo? Nati Samsoni kwa atate wace, Nditengereni iye, pakuti andikonda pamaso panga.

4 Koma atate wace ndi amai wace sanadziwa kuti cidacokera kwa Yehova ici; popeza analikufuna kutola cifukwa ndi Afilisti. Ndipo nthawi ija Afilisti analamulira Israyeli.

Samsoni apha mkango

5 Pamenepo anatsikira Samsoni, ndi atate wace ndi mai wace ku Timna, nadza ku minda yamphesa ya Timna; ndipo taona, mwana wa mkango wakomana naye namdzumira.

6 Ndipo unamgwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung'amba monga akadang'amba mwana wa mbuzi, wopandakanthu m'dzanjaliace; koma sanauza atate wace kapena amai wace cimene adacicita.

7 Ndipo anatsika nakamba ndi mkazi, namkonda Samsoni pamaso pace.

8 Atapita masiku ndipo anabweranso kudzamtenga, napambuka iye kukaona mtembo wa mkango; ndipo taona, m'citanda ca mkango munali njuci zoundana, ndi uci.

9 Ndipo anaufula ndi dzanja lace, nayenda, namadya alimkuyenda, nadza kwa atate wace ndi amai wace, nawapatsa, nadya iwo; koma sanawauza kuti adaufula uciwo m'citanda ca mkango.

Awaphera anthu mwambi

10 Ndipo atate wace anatsikira kwa mkazi; ndi Samsoni anakonzerapo madyerero; pakuti amatero anyamata.

11 Ndipo kunali, pamene anamuona, anabwera nao anzace makumi atatu akhale naye.

12 Nanena nao Samsoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kuukumika uwu, ndidzakupatsani malaya a nsaru yabafuta makumi atatu, ndi zobvala zosinthanitsa makumi atatu;

13 koma ngati simukhoza kunditanthauzira uwu mudzandipatsa ndinu Malaya a nsaru yabafuta makumi atatu ndi zobvala zosinthanitsa makumi atatu. Pamenepo ananena naye, Mwambi wako tiumve.

14 Ndipo ananena nao,Cakudya cinaturuka m'mwini kudya,Ndi cozuna cinaturuka m'mwini mphamvu,Ndipo masiku atatu sanakhoza kutanthauzira mwambiwo.

15 Koma kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri anati kwa mkazi wa Samsoni, Kopa mwamuna wako, atitanthauzire mwambiwo; tingatenthe iwe ndi nyumba ya atate wako ndi mota. Kodi mwatiitana kulanda zathu; si momwemo?

16 Ndipo mkazi wa Samsoni analira pamaso pace, nati, Ungondida, osandikonda; waphera anthu a mtundu wanga mwambi, osanditanthauzira ine. Ndipo ananena naye, Taona, sindinatanthauzira atate wanga kapena amai wanga, kodi ndikutanthauzire iwe?

17 Ndipo analira pamaso pace masiku asanu ndi awiriwo pocitika madyerero ao; koma kunali kuti tsiku lacisanu ndi ciwiri anamuuza, popeza anamuumiriza; ndipo anatanthauzira anthu a mtundu wace mwambiwo.

18 Ndipo amuna a pamudzi anati kwa Samsoni tsiku lacisanu ndi ciwiri, lisanalowe dzuwa, Cozuna coposa uci nciani; ndi camphamvu coposa mkango nciani? Pamenepo ananena nao,Mukadapanda kulima ndimthandi wanga,Simukadakumika mwambi wanga.

19 Ndipo mzimu wa Yehova unamgwera Samsoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zobvala zao, nawapatsa okumika mwambiwo zobvala zosinthanitsa. Koma adapsa mtima, nakwera kumka ku nyumba ya atate wace.

20 Ndipo mkazi wace wa Samsoni anakhala wa mnzace, amene adakhala bwenzi lace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21