Oweruza 11 BL92

Yefita alanditsa Israyeli

1 Yefita Mgileadi ndipo anali ngwazi yamphamvu, ndiye mwana wa mkazi wadama; koma Gileadi adabala Yefita.

2 Ndipo mkazi wa Gileadi anambalira ana amuna; koma atakula ana amuna a mkaziyo anampitikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira colowa m'nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina.

3 Pamenepo Yefita anathawa abale ace, nakhala m'dziko la Tobu; ndipo anyamata opanda pace anasonkhana kwa Yefita, naturuka naye pamodzi.

4 Ndipo kunali, atapita masiku, ana a Amoni anacita nkhondo ndi Israyeli,

5 ndipo kunatero, pamene ana a Amoni anathira nkhondo pa Israyeli, akuru a Gileadi anamuka kutenga Yefita m'dziko la Tobu;

6 nati kwa Yefita, Tiye ukhale kazembe wathu kuti tilimbane ndi ana a Amoni.

7 Ndipo Yefita anati kwa akulu a Gileadi, Simunandida kodi, ndi kundicotsa m'nyumba ya atate wanga? ndipo mundidzeraoji tsopano pokhala muli m'kusauka?

8 Ndipo akuru a Gileadi ananena ndi Yefita, Cifukwa cace cakuti takubwerera tsopano ndico kuti umuke nafe ndi kucita nkhondo ndi ana a Amoni, nudzakhala mkuru wathu wa pa onse okhala m'Gileadi.

9 Ndipo Yefita anati kwa akuru a Gileadi, Mukaodifikitsanso kwathu kucita nkhondo ndi ana a Amoni, nakawapereka Yehova pamaso panga, ndidzakhala mkuru wanu kodi?

10 Ndipo akuru a Gileadi anati kwa Yefita, Yehova ndiye wakumvera pakati pa ife, tikapanda kucita monga momwe wanena.

11 Pamenepo Yefita anamuka ndi akuru a Gileadi, ndipo anthu anamuika mkuru wao ndi mtsogoleri wao; ndipo Yefita ananena mau ace onse pamaso pa Yehova ku Mizipa.

12 Ndipo Yefita anatuma mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kuti, Ndi ciani ndi Inu, ndi kuti Mwandidzera kuthira nkhondo dziko langa?

13 Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Cifukwa Israyeli analanda dziko langa pakukwera iye kucokera ku Aigupto, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordano; ndipo tsopano uodibwezere maikowa mwamtendere.

14 Ndipo Yefita anatumanso mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni;

15 nanena naye, Atero Yefita, Israyeli sanalanda dziko la Moabu kapena dziko la ana a Amoni;

16 pakuti pakukwera iwo kucokera ku Aigupto Israyeli anayenda m'cipululu mpaka Nyanja Yofiira, nafika ku Kadesi;

17 pamenepo Israyeli anatuma mithenga kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Ndikupemphani ndipitire pakati pa dziko lanu; koma mfumu ya Edomu sinamvera. Natumanso kwa mfumu ya Moabu; nayenso osalola; ndipo Israyeli anakhala m'Kadesi.

18 Pamenepo anayenda m'cipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Moabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Moabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Moabu, pakuti Arinoni ndi malire a Moabu.

19 Ndipo Israyeli anatuma mithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, mfumu ya ku Hesiboni; nanena naye Israyeli, Tikupemphani tipitire pakati pa dziko lanu, kumka kwathu.

20 Koma Sihoni sanakhulupirira Israyeli kuti apitire pakati pa malire ace; koma Sihoni anamemeza anthu ace onse, namanga misasa ku Yahazi, nathira nkhondo Israyeli.

21 Ndipo Yehova Mulungu wa Israyeli anapereka Sihoni ndi anthu ace onse m'dzanja la Israyeli, ndipo anawakantha, ndi Israyeli analandira colowa cace, dziko lonse la Aamori, nzika za m'dziko lija.

22 Ndipo analandira akhale colowa cao, malire onse a Aamori, kuyambira Arihoni mpaka Yaboki, ndi kuyambira cipululu mpaka Yordano.

23 Motero Yehova Mulungu wa Israyeli anaingitsa Aamori, pamaso pa anthu ace Israyeli, ndipo kodi liyenera kukhala colowa canu?

24 Cimene akulandiritsani Kemosi mulungu wanu, simucilandira colowa canu kodi? Momwemo ali yense Yehova Mulungu wathu waiogitsa pamaso pathu, zacezo tilandira colowa cathu.

25 Ndipo tsopano kodi inu ndinu wabwino woposa Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Moabu; anatengana konse ndi Israyeli iyeyu kodi, kapena kucita nao nkhondo konse kodi?

26 Pokhala Israyeli m'Hesiboni ndi midzi yace, ndi m'Aroeri ndi midzi yace, ndi m'midzi yonse yokhala m'mphepete mwa Arinoni zaka mazana atatu; munalekeranji kulandanso nthawi ija?

27 Potero sindinakucimwirani ine, koma mundicitira coipa ndinu kundithira nkhondo; Yehova, Woweruzayo, aweruze lero lino pakati pa ana a Israyeli ndi ana a Amoni.

28 Koma mfumu ya ana a Amoni sanamvera mau a Yefita anamtumizirawo.

Cowinda ca Yefita

29 Pamenepo mzimu wa Yehova unamdzera Yefita, napitira iye ku Gileadi, ndi Manase, napitira ku Mizipa wa Gileadi, ndi kucokera ku Mizipa wa Gileadi anapitira kwa ana a Amoni.

30 Ndipo Yefita anawindira Yehova cowinda, nati, Mukaperekatu ana a Amoni m'dzanja langa, ndipo kudzali kuti ciri conse cakuturuka pakhomo pa nyumba yanga kudzakomana nane pakubweranso ine ndi mtendere kucokera kwa ana a Amoni, cidzakhala ca Yehova, ndipo ndidzacipereka nsembe yopsereza.

32 Potero Yefita anapita kwa ana a Amoni kuwathira nkhondo; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja lace;

33 nawakantha kuyambira ku Aroeri mpaka ufika ku Miniti, ndiyo midzi makumi awiri, ndi ku Abelikerami, makanthidwe akuru ndithu. Motero ana a Amoni anagonjetsedwa pamaso pa ana a Israyeli.

34 Pofika Yefita ku Mizipa ku nyumba yace, taonani, mwana wace wamkazi anaturuka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe; ndipo iyeyu anali mwana wace mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.

35 Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zobvala zace, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukuru, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.

36 Ndipo anati kwa iye, Atate wanga, mwamtsegulira Yehova pakamwa panu, mundicitire ine monga umo mudaturutsa mau pakamwa panu; popeza Yehova anakucitirani inu cilango pa adani anu, pa ana a Amoni.

37 Ndipo anati kwa atate wace, Andicitire ici, andileke miyezi iwiri, kuti ndicoke ndi kutsikira kumapiri, ndi kulirira unamwali wanga, ine ndi anzanga.

38 Nati iye, Muka. Namuuza amuke akakhale miyezi iwiri; namuka iye ndi anzace, nalirira unamwali wace pamapiri.

39 Ndipo kunali pakutha miyezi iwiri, anabwerera kwa atate wace amene anamcitira monga mwa cowinda cace anaciwinda; ndipo sanamdziwa mwamuna. Motero unali mwambo m'Israyeli,

40 kuti ana akazi a Israyeli akamuka caka ndi caka kumliririra mwana wa Yefita wa ku Gileadi, masiku anai pa caka.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21