Oweruza 13 BL92

Aisrayeli agonjera Afilisti; abadwa Samsoni

1 Ndipo ana a Israyeli anaonjeza kucita coipa pamaso pa Yehova; nawapereka Yehova m'dzanja la Afilisti zaka makumi anai.

2 Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lace ndiye Manowa; ndi mkazi wace analibe mwana, sanabala.

3 Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana, wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna.

4 Cifukwa cace udzisamalire, usamwe vinyo kapena coledzeretsa, nusadye cinthu ciri conse codetsa;

5 pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pace sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri cibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israyeli m'dzanja la Afilisti.

6 Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wace ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ace ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunsa uko acokera kapena sanandiuzanso dzina lace;

7 koma anati kwa ine, Taona, udzaima, ndi kubala mwana wamwamuna; ndipo tsopano usamwe vinyo kapena coledzeretsa, nusadye ciri conse codetsa; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri cibadwire mpaka tsiku la kufa kwace.

8 Pamenepo Manowa anapembedza Yehova, nati, Yehova, ndikupemphani, atidzerenso munthu wa Mulungu mudamtumayo, natilangize ico tizicitira mwanayo akadzabadwa.

9 Ndipo Mulungu anamvera mau a Manowa; ndi mthenga wa Mulungu anamdzeranso mkaziyo, pamene anali m'munda, mwanuna wace Manowa palibe.

10 Ndipo mkaziyo anafulumira nathamanga, nauza mwamuna wace, nanena naye, Taona, wandionekera munthu anandidzerayo tsiku lija.

11 Nanyamuka Manowa natsata mkazi wace, namdzera mwamuna uja, nanena naye, Kodi ndinu mwamuna ujamunalankhulandimkaziyu? Ndipo anati, Ndine amene.

12 Nati Manowa, Acitike tsopano mau anu; koma makhalidwe ace a mwanayo ndi macitidwe ace adzatani?

13 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Zonse ndinazinena ndi mkazi azisamalire.

14 Ciri conse cicokera kumpesa asadyeko, asamwe vinyo kapena coledzeretsa, kapena kudya ciri conse codetsa; zonse ndinamlamulira azisunge.

15 Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Tiloleni tikucedwetseni kuti tikukonzereni mwana wa mbuzi.

16 Koma mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Ungakhale undicedwetsa, sindidzadya mkate wako; ndipo ukakonza nsembe yopsereza, uziipereka kwa Yehova. Pakuti Manowa sanadziwa kuti ndiye mthenga wa Yehova.

17 Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Dzina lanu ndani, kuti, atacitika mau anu, tikucitireni ulemu.

18 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ufunsiranji dzina langa, popeza liri lodabwitsa?

19 Pamenepo Manowa anatenga mwana wa mbuzi pamodzi ndi nsembe yaufa, nazipereka kwa Yehova pathanthwe; ndipo mthengayo anacita modabwitsa, ndi Manowa ndi mkazi wace ali cipenyereo

20 Pakuti kunali, pakukwera lawi la mota pa guwa la nsembe kumwamba, mthenga wa Yehova anakwera m'lawi la pa guwalo; ndi Manowa ndi mkazi wace ali cipenyere; nagwa iwowa nkhope zao pansi.

21 Ndipo mthenga wa Yehova sanaonekeranso kwa Manowa kapena kwa mkazi wace. Pamenepo anadziwa Manowa kuti ndiye mthenga wa Yehova.

22 Nati Manowa kwa mkazi wace, Tidzafa ndithu pakuti taona Mulungu.

23 Koma mkazi wace ananena naye, Yehova akadafuna kutipha, sakadalandira nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa pa dzanja lathu, kapena kutionetsa izi zonse, kapena kutimvetsa zoterezi nthawi yino.

24 Ndipo mkaziyo anabala mwana wamwamuna namucha dzina lace Samsoni; nakula mwanayo, Yehova namdalitsa.

25 Ndipo mzimu wa Yehova unayamba kumfulumiza mtima ku misasa ya Dani pakati pa Zora ndi Esitaoli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21