1 Ndipo ana a Israyeli anaonjeza kucita coipa pamaso pa Yehova, atafa Ehudi.
2 Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wocita ufumu ku Hazori; kazembe wace wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu.
3 Ndipo ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova; pakuti anali nao magareta acitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israyeli kolimba zaka makumi awiri.
4 Ndipo Debora, mneneri wamkazi, ndiye mkazi wace wa Lapidoti, anaweruza Israyeli nyengo ija,
5 Ndipo anakhala patsinde pa mgwalangwa wa Debora pakati pa Rama ndi Beteli ku mapiri a Efraimu; ndi ana a Israyeli anakwera kwa iye awaweruze.
6 Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinoamu, acoke m'Kedesi-Nafitali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israyeli sanalamulira ndi kuti, Muka, nuluniike ku phiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafitali ndi ana a Zebuloni?
7 Ndipo ndidzamkoka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere ku mtsinje wa Kisoni, ndi magareta ace, ndi aunyinji ace; ndipo ndidzampereka m'dzanja lako.
8 Ndipo Baraki anati kwa iye, Ukamuka nane, ndidzamuka; ukapanda kumuka nane, sindimuka.
9 Nati iye, Kumuka ndidzamuka nawe, koma ulendo umukawo, sudzacita nao ulemu; pakuti: Yehova adzagulitsa Sisera m'dzanja la mkazi, Motero Debora anauka namuka ndi Baraki ku Kedesi.
10 Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafitali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kumka naye.
11 Ndipo Heberi Mkeni anadzisiyanitsa ndi Akeni, ndi ana a Hobabu mlamu wace wa Mose, namanga mahema ace mpaka thundu wa m'Zaananimu, ndiwo wa ku Kedesi.
12 Ndipo anauza Sisera kuti Baraki mwana wa Abinoamu wakwera ku phiri la Tabori.
13 Pamenepo Sisera anasonkhanitsa magareta ace onse ndiwo magareta mazana asanu ndi anai acitsulo, ndi anthu onse okhala naye, kuyambira Haroseti wa amitundu mpaka mtsinje wa Kisoni.
14 Ndipo Debora anati kwa Baraki, Nyamuka; pakuti ili ndi tsikuli Yehova wapereka Sisera m'dzanja lako; sanaturuka kodi Yehova pamaso pako? Potero Baraki anatsika ku phiri la Tabori ndi amuna zikwi khumi akumtsata.
15 Ndipo Ambuye anaononga Sisera, ndi magareta onse ndi gulu lankhondo lonse, adi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagareta nathawa coyenda pansi.
16 Koma Baraki anatsata magareta ndi gululo mpaka Haroseti wa amitundu; ndi gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa, sanatsala munthu ndi mmodzi yense.
17 Koma Sisera anathawira coyenda pansi ku hema wa Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni; pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori, ndi nyumba ya Heberi Mkeni.
18 Ndipo Yaeli anaturuka kukomana ndi Sisera, nanena naye, Pambuka, mbuye wanga, pambukira kwa ine kuno; usaope. Ndipo anapambukira kwa iye kulowa m'hema, nampfunda ndi cimbwi.
19 Pamenepo ananena naye, Ndipatsetu madzi pang'ono ndimwe; popeza ndine waludzu. Ndipo anatsegula thumba la mkaka, nampatsa amwe, nampfunda.
20 Ndipo Sisera ananena naye, Taima pakhomo pa hema, ndipo kudzali, akadza munthu, akakufunsa akati, Pali munthu pano kodi? Uziti, Palibe.
21 Pamenepo Yaeli mkazi wa Heberi anatenga ciciri ca hema, natenga nyundo m'dzanja lace namdzera monyang'ama, nakhomera ciciri cilowe m'litsipa mwace; nicinapyoza kulowa m'nthaka; popeza anali m'tulo tofa nato ndi kulema; nafa.
22 Ndipo taonani, pomlondola Sisera Barakiyo, Yaeli anaturuka kukomana naye, Dati kwa iye, Idza kuno, ndidzakuonetsa munthu umfunayo, Potero anamdzera, ndipo taonani, Sisera wagwa, wafa, ndi ciciri m'litsipa mwace.
23 Momwemo Mulungu anagonjetsa tsiku lija Yabini mfumu ya Kanani pamaso pa ana a Israyeli.
24 Ndipo dzanja la ana a Israyeli linamkabe ndi kulimbika pa Yabini mfumu ya Kanani mpaka adamuononga Yabini mfumu ya Kanani.