Oweruza 15 BL92

Samsoni atentha za m'minda ya Afilisti

1 Ndipo kunali atapita masiku, nyengo ya kuceka tirigu Samsoni anakaceza ndi mkazi wace ndi kumtengera mbuzi, nati, Ndidzalowa kwa mkazi wanga kucipinda. Koma atate wace sanamlola kulowamo.

2 Nati atate wace, Ndinanenetsa kuti umuda konse, potero ndinampereka kwa bwenzi tako; mng'ono wace sakoma koposa iye nanga? ukhale naye, m'malo mwa winayu.

3 Koma Samsoni ananena nao, Nthawi yino ndikhala wosaparamula pa Afilisti, powacitira coipa ine.

4 Namuka Samsoni, nagwira ankhandwe mazana atatu, natenga miuni, nalunza micira, naika muuni pakati pa micira iwiri iri yonse.

5 Nayatsa miuni, nawataya ku tirigu wosaceka wa Afilisti, natentha miulu ndi tirigu wosaceka yemwe, ndi minda ya azitona yomwe.

6 Pamenepo Afilisti anati, Wacita ici ndani? Nati, Samsoni mkamwini wa munthuyo wa ku Timna, popeza analanda mkazi wace, nampereka kwa mnzace. Pamenepo Afilisti anakwera namtentha mkaziyo ndi atate wace ndi moto.

7 Ndipo Samsoni ananena nao, Mukatero ndidzakubwezerani cilango ndi pamenepo ndidzaleka.

8 Ndipo anawakantha nyung'unyu ndi ncafu, makanthidwe akuru; natsika nakhala m'phanga mwa thanthwe la ku Etamu.

Ayesa kumanga Samsoni, napha ive anthu ambiri

9 Pamenepo Afilisti anakwera, namanga misasa m'Yuda, natandika m'Leki

10 Ndipo anthu a Yuda anati, Mwatikwerera cifukwa ninji? Nati iwo, Takwera kumanga Samsoni, kumcitira iye monga anaticitira ife.

11 Pamenepo anatsikira ku phanga la Etamu amuna zikwi zitatu, nati kwa Samsoni, Sudziwa kodi kuti Atilisti ndiwo akutilamulira ife? nciani ici waticitira? Nati iye kwa iwowa, Monga anandicitira ine ndawacitira iwo.

12 Ndipo ananena naye, Tatsika ife tikumange, kuti tikupereke m'dzanja la Atilisti. Nanena nao Samsoni, Mundilumbirire kuti simudzandigwera nokha.

13 Ndipo anati kwa iye, Iai, koma kumanga tidzakumanga, ndi kukupereka m'dzanja lao; koma kupha sitikupha iwe. Nammanga iye ndi zingwe ziwiri zatsopano, nakwera naye kucokera kuthanthwe.

14 Pamene anafika ku Leki Afilisti anapfuula pokomana naye; koma mzimu wa Yehova unamgwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ace zinanga bwazi lopserera ndi moto, ndi zomangira zace zinanyotsoka pa manja ace.

15 Ndipo anapeza cibwano catsopano ca buru, natambasula dzanja lace nacigwira, nakantha naco amuna cikwi cimodzi.

16 Nati Samsoni,Ndi cibwano ca buru, miuru miuru,Amuna cikwi ndawakantha ndi cibwano ca buru.

17 Ndipo kunali, atatha kunena, anataya cibwano m'dzanja lace; nawacha maiowo Ramati-leki ndiko kunena citunda ca cibwano.

18 Ndipo anamva ludzu lambiri, naitana kwa Yehova, nati, Mwapatsa Inu cipulumutso ici cacikuru ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m'dzanja la osadulidwa awa?

19 Pamenepo Mulungu anang'amba pokumbika paja pit Leki, naturukamo madzi; namwa iye, nubwera moyo wace, natsitsimuka iye; cifukwa cace anawacha dzina lace, Kasupe wa wopfuula, ndiwo m'Leki mpaka lero lino.

20 Ndipo Samsoni anaweruza Israyeli m'masiku a Afilisti zaka makumi awiri.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21