Oweruza 1 BL92

Aisrayeli aonjeza kugonjetsa Akanani

1 NDIPO atafa Yoswa, ana a Israyeli anafunsira kwa Yehova ndi kuti, Adzayamba ndani kutikwerera pa Akanani kuwathira nkhondo?

2 Ndipo Yehova anati, Akwere Yuda; taonani, ndapereka dzikoli m'dzanja lace.

3 Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkuru wace, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni.

4 Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m'dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi.

5 Ndipo anapeza Adoni-bezeki m'Bezeki, namthira nkhondo nakantha Akanani ndi Aperizi.

6 Koma Adoni-bezeki anathawa; ndipo anampitikitsa, namgwira, namdula zala zazikuru za m'manja ndi za m'mapazi.

7 Pamenepo anati Adoni-bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikuru za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinacita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.

8 Ndipo ana a Yuda anacita nkhondo pa Yerusalemu, naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi ndi moto.

9 Ndipo atatero ana a Yuda anatsika kuthirana nao nkhondo Akanani akukhala kumapiri, ndi kumwela ndi kucidikha.

10 Ndipo Yuda anamuka kwa Akanani akukhala m'Hebroni; koma kale dzina la Hebroni ndilo mudzi wa Ariba; ndipo anakantha Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai.

11 Pocoka pamenepo anamuka kwa nzika za ku Dibiri, koma kale dzina la Dibiri ndilo mudzi wa Seferi.

12 Ndipo Kalebe anati, iye amene akantha mudzi wa Seferi, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga wamkazi akhale mkazi wace.

13 Ndipo Otiniyeli, mwana wa Kenazi mng'ono wa Kalebi anaulanda, ndipo anampatsa Akisa mwana wace wamkazi akhale mkazi wace.

14 Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkakamiza mwamuna wace kuti apemphe atate wace ampatse munda; natsika pa buru wace; ndipo Kalebe ananena naye, Ufunanji?

15 Ndipo anati kwa Iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko lakumwela, ndipatsenso zitsime za madzi. Pamenepo Kalebe anampatsa zitsime za kumtunda ndi zitsime za kunsi.

16 Ndipo ana a Mkeni mlamu wace wa Mose, anakwera kuturuka m'mudzi wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'cipululu ca Yuda cokhala kumwela kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.

17 Ndipo Yuda anamuka ndi Simeoni mkuru wace, nakantha Akanani akukhala m'Zefati, nauononga konse. Koma dzina la mudziwo analicha Horima.

18 Yuda analandanso Gaza ndi malire ace, ndi Asikeloni ndi malire ace, ndi Ekroni ndi malire ace.

19 Ndipo Yehova anali ndi Yuda, iye nawaingitsa a kumapiri, osaingitsanzika za kucigwa, popeza zinali nao magareta acitsulo.

20 Ndipo anapatsa Kalebe Hebroni monga Mose adanena; iye nawaingitsa komweko ana amuna atatu a Anaki.

21 Koma ana a Benjamini sanaingitsa Ayebusi okhala m'Yerusalemu; koma Ayebusi anakhala m'Yerusalemu pamodzi ndi ana a Benjamini, mpaka lero lino.

22 Ndipo anakwera iwo a m'nyumba ya Yosefe naonso kumka ku Beteli; ndipo Yehova anakhala nao.

23 Ndipo iwo a m'nyumba ya Yosefe anatumiza ozonda ku Beteli. Koma kale dzina la mudziwo ndilo Luzi.

24 Ndipo alonda anaona munthu alikuturuka m'mudzi, nanena naye, Utionetsetu nolowera m'mudzi, ndipo tidzakucitira cifundo.

25 Nawaonetsa polowera m'mudzi iye, naukantha mudzi iwowa ndi lupanga lakuthwa; koma analola munthuyo ndi banja lace lonse amuke.

26 Ndipo munthuyo anamuka ku dziko la Ahiti, namanga mudzi, naucha dzina lace Luzi; ndilo dzina lace mpaka lero lino.

Aisrayeli aleka kugonjetsa Akanani ena

27 Koma Manase sanaingitsa a ku Betiseani ndi midzi yace kapena a Taanaki ndi midzi yace, kapena nzika za ku Dori ndi midzi yace, kapena nzika za ku Ibleamu ndi midzi yace, kapena nzika za ku Megido ndi midzi yace; koma Akanani anakhumba kukhala m'dziko muja.

28 Ndipo kunali, atakula mphamvu Israyeli, anasonkhetsa Akanani, osawaingitsa onse.

29 Ndipo Efraimu sanaingitsa Akanani okhala m'Gezeri; koma Akanani anakhala m'Gezeri pakati pao,

30 Zebuloni sanaingitsa nzika za ku Kitroni, kapena nzika za ku Nahaloli; koma Akanaru anakhala pakati pao, nawasonkhera.

31 Aseri sanaingitsa nzika za ku Ako, kapena nzika za ku Sidoni, kapena a Akalabu, kapena a Akisibu, kapena a Heliba, kapena a Afiki, kapena a Rehobo;

32 koma Aseri anakhala pakati pa Akanani nzika za kudziko; pakuti sanawaingitsa.

33 Nafitali sanaingitsa nzika za ku Beti-semesi, kapena nzika za ku Beri-anati; koma anakhala pakati pa Akanani, nzika za kudziko; koma nzika za ku Beti-semesi, ndi a ku Beti-anati zinawasonkhera.

34 Ndipo Aamori anakankha ana a Dani akhale kumapiri pakuti sanawalola atsikire kucigwa;

35 Aamori anakhumbanso kukhala ku phiri la Heresi, ku Ajaloni, ndi ku Saalibimu; koma dzanja la a m'nyumba ya Yosefe linawalaka, nakhala iwo akupereka msonkho.

36 Ndipo malire a Aamori anayambira pokwerera pa Akrabimu, pathanthwe, ndi pokwererapo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21