Yoswa 24 BL92

Yoswa akumbutsa anthu zowacitira Mulungu

1 Ndipo Yoswa anasonkhanitsa mapfuko onse a Israyeli ku Sekemu, naitana akulu akulu a Israyeli ndi akuru ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao; ndipo anadzilangiza pamaso pa Mulungu.

2 Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu yina iwowa.

3 Ndipo ndinamtenga kholo lanu Abrahamu tsidya lija la mtsinje, ndi kumuyendetsa m'dziko lonse la Kanani ndi kucurukitsa mbeu zace ndi kumpatsa Isake,

4 Ndi kwa Isake ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lace lace; koma Yakobo ndi ana ace anatsikira kumka ku Aigupto.

5 Pamenepo ndinatuma Mose ndi Aroni, ndipo ndinasautsa Aigupto, monga ndinacita pakati pace; ndipo nditatero ndinakuturutsani.

6 Ndipo ndinaturutsa atate anu m'Aigupto; ndipo munadzakunyanja; koma Aaigupto analondola atate anu ndi magareta ndi apakavalo mpaka ku Nyanja Yofiira.

7 Ndipo pamene anapfuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aaigupto nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya cocita Ine m'Aigupto; ndipo munakhala m'cipululu masiku ambiri.

8 Pamenepo ndinakulowetsani inu m'dziko la Aamori okhala tsidya lija la Yordano; nagwirana nanu iwowa; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu, nimunalandira dziko lao likhale lanu lanu; ndipo ndinawaononga pamaso panu.

9 Pamenepo Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Moabu, anauka naponyana ndi Israyeli; natuma naitana Balamu mwana wa Beori atemberere inu;

10 koma sindinafuna kumvera Balamu, potero anakudalitsani cidalitsire, ndipo ndinakulanelitsani m'dzanja lace.

11 Pamenepo munaoloka Yordano, ndi kufika ku Yeriko; ndi eni ace a ku Yeriko anaponyana nanu nkhondo, Aamori, ndi Aperizi, ndi Akanani, ndi Ahiti, ndi Agirigasi, Ahivi ndi Ayebusi; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu.

12 Ndipo ndinatuma mabvu atsogolere inu, amene anawaingitsa pamaso panu, ndiwo mafumu awiri a Aamori; osati ndi lupanga lako, kapena ndi uta wako ai.

13 Ndipo ndinakupatsani dziko limene simunagwiramo nchito, ndi midzi simunaimanga, ndipo mukhala m'mwemo; mukudya za m'minda yamphesa, ndi minda yaazitona imene simunaioka.

Yoswa abwereza kucita pangano pakati pa Mulungu ndi anthu

14 Ndipo tsopano, opani Yehova ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro ndi woona; nimucotse milungu imene makolo anu anaitumikira tsidya lija la mtsinje, ndi m'Aigupto; nimutumikire Yehova.

15 Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.

16 Ndipo anthu anayankha, nati, Sikungatheke kuti timsiye Yehova, ndi kutumikira milungu yina;

17 pakuti Yehova Mulungu wathu ndi iye amene anatikweza kutiturutsa m'dziko la Aigupto ku nyumba ya akapolo, nacita zodabwiza zazikuruzo pamaso pathu, natisunga m'njira monse tidayendamo, ndi pakati pa anthu onse amene tinapita pakati pao;

18 ndipo Yehova anaingitsa pamaso pathu anthu awa onse, ngakhale Aamori okhala m'dzikomo; cifukwa cace ifenso tidzatumikira Yehova, pakuti ndiye Mulungu wathu.

19 Ndipo Yoswa anati kwa anthu, Simukhoza inu kutumikira Yehova pakuti ndiye Mulungu woyera, ndi Mulungu wansanje; sadzalekerera zolakwa zanu, kapena zocimwa zanu.

20 Mukasiya Yehova, ndi kutumikira milungu yacilendo, adzatembenuka ndi kukucitirani coipa, ndi kukuthani, angakhale anakucitirani cokoma.

21 Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Iaitu, koma tidzatumikira Yehova.

22 Ndipo Yoswa ananena ndi anthu, Inu mwadzicitira mboni inu nokha kuti mwadzisankhira Yehova kumtumikira iye. Ndipo anati, Ndife mboni.

23 Ndipo tsopano, cotsani milungu yacilendo iri pakati pa inu, ndi kulozetsa mitima yanu kwa Yehova, Mulungu wa Israyeli.

24 Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Tidzamtumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera mau ace.

25 Motero Yoswa anacita pangano ndi anthu tsiku lija, nawaikira lemba ndi ciweruzo m'Sekemu.

26 Ndipo Yoswa analembera mau awa m'buku la cilamulo ca Mulungu; natenga mwala waukuru, nauimitsa apo patsinde pa thundu wokhala pa malo opatulika a Yehova.

27 Ndipo Yoswa anati kwa anthu onse, Taonani, mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa; pakuti udamva mau onse a Yehova amene ananena kwa ife; ndipo udzakhala mboni yotsutsa inu, mungakanize Mulungu wanu.

28 Pamenepo Yoswa anauza anthu amuke, yense ku colowa cace.

Amwalira Yoswa ndi Eleazare

29 Ndipo kunali, zitatha izi, Yoswa mwana wa Nuni mtumiki wa Yehova, adafa, wa zaka zana ndi khumi.

30 Ndipo anamuika m'malire a colowa cace m'Timinati-sera, ndiwo ku mapiri a Efraimu kumpoto kwa phiri la Gaasi.

31 Ndipo Israyeli anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akulu akulu otsala atafa Yoswa, amene anadziwa nchito yonse ya Yehova anaicitira Israyeli.

32 Ndipo mafupa a Yosefe amene ana a Israyeli anakwera nao kucokera ku Aigupto anawaika ku Sekemu, pa kadziko kamene adakagula Yakobo kwa ana a Hamori atate wa Sekemu ndi kuwapatsa ndalama zana; ndipo anakhala colowa ca ana a Yosefe.

33 Eleazarenso mwana wa Aroni anafa; ndipo anamuika pa phiri la Pinehasi mwana wace, limene adampatsa ku mapiri a Efraimu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24