Yoswa 23 BL92

Yoswa acenjeza anthu asunge Malamulo a Mulungu

1 Ndipo atapita masiku ambiri, Yehova atapumulitsa Israyeli kwa adani ao onse akuwazungulira, ndipo Yoswa adakalamba nakhala wa zaka zambiri;

2 Yoswa anaitana Aisrayeli onse, akulu akulu ao, ndi akuru ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao, nanena nao, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri;

3 ndipo munapenya zonse Yehova Mulungu anacitira mitundu iyi yonse ya anthu cifukwa ca inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo.

4 Taonani, ndakugawirani mitundu ya anthu iyi yotsala ikhale colowa ca mapfuko anu, kuyambira ku Yordano, ndi mitundu yonse ya anthu ndinaipasula, mpaka ku nyanja yaikuru ku malowero a dzuwa.

5 Ndipo Yehova Mulungu wanu Iyeyu adzawapitikitsa pamaso panu, ndi kulanda dziko lao kuwacotsa pamaso panu, ndipo mudzalandira dziko lao likhale colowa canu; monga Yehova Mulungu wanu ananena ndi inu.

6 Koma mulimbike mtima kwambiri kusunga ndi kucita zonse zolembedwa m'buku la cilamulo ca Mose, osacipambukira kulamanja kapena kulamanzere;

7 osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kuchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;

8 koma muumirire Yehova Mulungu wanu, monga munacita mpaka lero lino.

9 Pakuti Yehova anaingitsa pamaso panu mitundu yaikuru ndi yamphamvu; koma inu, palibe munthu anaima pamaso panu mpaka lero lino.

10 Munthu mmodzi wa inu adzapitikitsa anthu cikwi cimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.

11 Potero mudzisamalire ndithu kuti mukonde Yehova Mulungu wanu.

12 Koma, mukadzabwereram'mbuyo pang'ono pokha ndi kuumirira otsala a mitundu awa, ndiwo akutsala pakati pa inu, ndi kukwatitsana nao, ndi kulowana nao, naonso kulowana nanu;

13 dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwacotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m'nthiti mwanu, ndi minga m'maso mwanu, mpaka mudzatayika m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.

14 Ndipo taonani, lero lino ndirikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m'mitima yanu yonse, ndi m'moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mau amodzi; onse anacitikira inu, sanasowapo mau amodzi.

15 Ndipo kudzakhala kuti monga zakugwerani zokoma zonse anakunenerani Yehova Mulungu wanu, momwemo Yehova adzakutengerani zoipa zonse mpaka atakuonongani kukucotsani m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.

16 Mukalakwira cipangano ca Yehova Mulungu wanu cimene analamulira inu ndi kumuka ndi kutumikira milungu yina ndi kuigwadira, mkwiyo wa Mulungu udzayakira inu, nimudzatayika msanga m'dziko lokomali anakupatsani.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24