Yoswa 10 BL92

Cinkhondo ku Gibeoni

1 Ndipo kunali, pamene Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anamva kuti Yoswa adalanda Ai, ndi kumuononga konse; nacitira Ai ndi mfumu yace monga adacitira Yeriko ndi mfumu yace; ndi kuti nzika za Gibeoni zinacitirana mtendere ndi Israyeli, nizikhala pakati pao;

2 anaopa kwambiri, popeza Gibeoni ndi mudzi waukuru, monga wina wa midzi yacifumu, popezanso unaposa Ai kukula kwace, ndi amuna ace onse ndiwo amphamvu.

3 Cifukwa cace Adoni-Zedeki anatuma kwa Hohamu, mfumu ya Hebroni, ndi kwa Piraniu mfumu ya Yarimutu, ndi kwa Yafiya mfumu ya Lakisi, ndi kwa Dibri mfumu va Egiloni, ndi kuti,

4 Kwerani kwanga kuno, ndi kundithandiza kuti tikanthe Gibeoni, pakuti unacitirana mtendere ndi Yoswa ndi ana a Israyeli.

5 Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimutu, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibeoni, nauthira nkhondo.

6 Ndipo amuna a ku Gibeoni anatumira Yoswa mau kucigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.

7 Pamenepo Yoswa anakwera kucokera ku Giligala, iye ndi anthu onse a nkhondo pamodzi naye, ndi ngwazi yose.

8 Ndipo Yehova ananena ndi Yoswa, Usawaope, pakuti ndawapereka m'dzanja lako; palibe mmodzi wa iwo adzaima pamaso pako.

9 Ndipo Yoswa anawadzidzimukitsa; popeza anakwera kucokera ku Giligala usiku wonse.

10 Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israyeli, ndipo anawakantha makanthidwe akuru ku Gibeoni, nawapitikitsa pa njira yokwera ya Betihoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda.

11 Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israyeli, potsikira pa Betihoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikuru yocokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anacuruka ndi iwo amene ana a Israyeli anawapha ndi lupanga.

Kuimitsidwa kwa dzuwa ndi mwezi

12 Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israyeli; ndipo anati pamaso pa Israyeli,Dzuwa iwe, linda, pa Gibeoni,Ndi Mwezi iwe, m'cigwa ca Aialo.

13 Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaimaMpaka anthu adabwezera cilango adani ao.Kodi ici sicilembedwa m'buku la Yasari? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu.

14 Ndipo panalibe tsiku lotere kale lonse kapena m'tsogolomo, lakuti Yehova anamvera mau a munthu; pakuti Yehova anathirira Israyeli nkhondo.

15 Pamenepo Yoswa anabwerera, ndi Aisrayeli onse pamodzi naye, ku cigono ca ku Giligala.

16 Ndipo mafumu awa asanu anathawa, nabisala m'phanga la ku Makeda,

17 Ndipo anauza Yoswa ndi kuti, Mafumu asanuwa apezeka obisala m'phanga la ku Makeda.

18 Ndipo Yoswa anati, Kunkhunizirani miyala yaikuru kukamwa kwa phanga, ndi kuikapo anthu, awasunge;

19 koma inu musaime, pitikitsani adani anu, ndi kukantha a m'mbuyo mwao; musawalole alowe m'midzi mwao; pakuti Yehova Mulungu wanu anawapereka m'dzanja lanu.

20 Ndipo kunali, Yoswa ndi ana a Israyeli atatha kuwakantha, makanthidwe akurukuru mpaka atatha psiti, ndipo otsala a iwo atalowa m'midzi ya malinga,

21 anthu onse anabwerera kucigono kwa Yoswa pa Makeda ndi mtendere. Palibe munthu anacitira cipongwe mmodzi yense wa ana a Israyeli.

22 Pamenepo Yoswa anati, Tsegula pakamwa pa phanga ndi kunditurutsira m'phanga mafumu asanuwo.

23 Ndipo anatero, naturutsira m'phanga mafumu asanuwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimutu, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni.

24 Ndipo kunali, ataturutsira Yoswa mafumu awa, Yoswa anaitana amuna onse a Israyeli, ndipo anati kwa akazembe a anthu a nkhondo amene anamuka naye, Yandikirani, pondani pa makosi a mafumu awa. Nayandikira iwo, naponda pa makosi ao.

25 Pamenepo Yoswa ananena nao, Musaope, musatenge nkhawa; khalani amphamvu, nimulimbike mtima; pakuti Yehova adzatero ndi adani: anu onse amene mugwirana nao: nkhondo.

26 Ndipo atatero, Yoswa anawakantha nawapha, nawapacika pa mitengo isanu; nalikupacikidwa pa mitengo mpaka madzulo.

27 Ndipo kunali, nthawi yakulowa dzuwa, Yoswa analamulira kuti awatsitse kumitengo; ndipo anawataya m'phanga m'mene adabisala; naika miyala yaikuru pakamwa pa phanga, mpaka lero lomwe lino.

Midzi ya kumwera igonja kwa Yoswa

28 Ndipo Yoswa anagwira Makeda tsiku lomwe lija ndi kuukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yace yom we; anawaononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, nacitira mfumu ya ku Makeda monga anacitira mfumu ya ku Yeriko.

29 Pamenepo Yoswa ndi Aisrayeli onse naye anapitirira kucokera ku Makeda kumka ku Libina, nathira nkhondo pa Libina;

30 ndipo Yehova anapereka uwunso, ndi mfumu yace m'dzanja la Israyeli; ndipo anaukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyamo ndi mmodzi yense; namcitira mfumu yace monga anacitira mfumu ya ku Yeriko.

31 Ndipo Yoswa, ndi Aisrayeli onse naye, anapitirira kucokera ku Libina kumka ku Lakisi; namanga misasa, nathira nkhondo pa uwo;

32 napereka Yehova Lakisi m'dzanja la Israyeli, ndipo anaulanda tsiku laciwiri, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo monga mwa zonse anacitira Libina.

33 Pamenepo Horamu mfumu ya Gezere anakwera kudzathandiza Lakisi; ndipo Yoswa anamkantha iye ndi anthu ace mpaka sanamsiyira ndi mmodzi yense.

34 Ndipo Yoswa, ndi Aisrayeli onse naye, anapitirira kucokera ku Lakisi mpaka ku Egiloni; namanga nrisasa, nathira nkhondo.

35 Naulanda tsiku lomwelo, naukantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse amoyo onse anali m'mwemo tsiku lomwelo, monga mwa zonse anacitira Lakisi.

36 Ndipo Yoswa ndi Aisrayeli onse naye anakwera kucokera ku Egiloni mpaka ku Hebroni, nauthira nkhondo;

37 naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yace ndi midzi yace yonse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, monga mwa zonse anacitira Egiloni; koma anauononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo.

38 Pamenepo Yoswa, ndi Aisrayeli onse naye, anabwerera kudza ku Dibiri, nauthira nkhondo,

39 naulanda, ndi mfumu yace ndi midzi yace yonse; naikantha ndi lupanga lakuthwa, naononga konse amoyo onse anali m'mwemo; sanasiya ndi mmodzi yense; monga anacitira Hebroni momwemo anacitira Dibiri ndi mfumu yace, monganso anacitira Libina ndi mfumu yace.

40 Motero Yoswa anakantha dziko lonse, la kumapiri, la kumwela, la kucidikha, la kuzigwa, ndi mafumu ao onse; sanasiyapo ndi mmodzi yense; koma anaononga psiti zonse zampweya, monga Yehova Mulungu wa Israyeli adalamulira.

41 Ndipo Yoswa anawakantha kuyambira Kadesi-Barinea mpaka ku Gaza, ndi dziko lonse la Goseni mpaka ku Gibeoni.

42 Ndipo Yoswa anagwira mafwnu awa onse ndi dziko lao nthawi yomweyi; cifukwa Yehova Mulungu wa Israyeli anathirira Israyeli nkhondo.

43 Pamenepo Yoswa ndi Aisrayeli onse naye, anabwerera kucigono ku Giligala.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24