Yoswa 7 BL92

Kucimwa kwa Akani

1 Koma ana a Israyeli analakwa ndi coperekedwaco; popeza Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa pfuko la Yuda, anatapa coperekedwaco; ndi mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Israyeli.

2 Ndipo Yoswa anatuma amuna kucokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Beti-aveni, kum'mawa kwa Beteli; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai.

3 Ndipo anabwera kwa Yoswa, nati kwa iye, Asakwere anthu onse; koma akwere amuna ngati zikwi ziwiri kapena zitatu kukantha Ai; musalemetsa anthu onse kumkako, pakuti a komweko ndi owerengeka;

4 Potero mwa anthu anakwerako amuna monga zikwi zitatu; koma anathawa pamaso pa amuna a ku Ai.

5 Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapitikitsa kuyambira pacipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.

6 Ndipo Yoswa anang'amba zobvala zace, nagwa nkhope yace pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akulu akulu a Israyeli, nathira pfumbi pamitu pao.

7 Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordano, kutipereka ife m'dzanja la Aamori, kutiononga ife? mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordano!

8 Ndidzanenanji, Ambuye, Israyeli atabwerera m'mbuyo pamaso pa adani ao?

9 Akadzamva ici Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu pa dziko lapansi; ndipo mudzacitiranji dzina lanu lalikuru?

10 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako cotere?

11 Israyeli wacimwa, nalakwiranso cipangano canga, ndinawalamuliraco; natengakonso coperekedwaco; anabanso, nanyenganso, naciika pakati pa akatundu ao.

12 Mwa ici ana a Israyeli sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga coperekedwaco, kucicotsa pakati pa inu.

13 Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Pali coperekedwa cionongeke pakati pako, Israyeli iwe; sukhoza kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutacotsa coperekedwaco pakati panu.

14 Koma m'mawa adzakuyandikitsani, pfuko ndi pfuko; ndipo kudzali kuti pfukoli Yehova aliulula lidzayandikira mwa zibale zace; ndi cibale Yehova aciulula cidzayandikira monga mwa a nyumba ace; ndi a m'nyumbawo Yehova awaulula adzayandikira mmodzi mmodzi.

15 Ndipo kudzali kuti iye wogwidwa ali naco coperekedwaco adzatenthedwa ndi moto, iye ndi zonse ali nazo cifukwa analakwira cipangano ca Yehova, ndi cifukwa anacita copusa m'Israyeli.

16 Ndipo Yoswa analawira mamawa, nayandikizitsa Israyeli, pfuko ndi pfuko; ndi pfuko la Yuda linagwidwa;

17 nayandikizitsa zibale za Yuda, nagwira cibale ca Azari; nayandikizitsa cibale ca Azari, mmodzi mmodzi, nagwidwa Zabidi;

18 nayandikizitsa a m'nyumba yace mmodzi mmodzi; ndipo Akani, mwana wa Karimu, mwanu wa Zabidi, mwana wa Zera, wa pfuko la Yuda anagwidwa.

19 Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, ucitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israyeli, numlemekeze iye; nundiuze tsopano, wacitanji? usandibisire.

20 Ndipo Akani anayankha Yoswa nati, Zoonadi, ndacimwira Yehova Mulungu wa Israyeli, ndacita zakuti zakuti;

21 pamene ndinaona pazofunkha maraya abwino a ku Babulo, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi cikute cagolidi, kulemera kwace masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pacepo.

22 Pamenepo Yoswa anatuma mithenga, iwo nathamangira kuhema; ndipo taonani, zidabisika m'hema mwace ndi siliva pansi pace.

23 Ndipo anazicotsa pakati pa hema, nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa ana onse a Israyeli, nazitula pamaso pa Yehova.

24 Ndipo Yoswa, ndi Aisrayeli onse naye, anatenga Akani mwana wa Zera, ndi siliva, ndi marayawo, ndi cikute cagolidi, ndi ana ace amuna ndi akazi, ndi ng'ombe zace, ndi aburu ace, ndi nkhosa zace, ndi hema wace ndi zace zonse; nakwera nazo ku cigwa ca Akori.

25 Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo, Aisrayeli onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto, nawaponya miyala.

26 Ndipo anamuuniikira mulu waukuru wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wace waukuru. Cifukwa cace anacha dzina lace la malowo, Cigwa ca Akori, mpaka lero lino.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24