Yoswa 13 BL92

Cigawo ca dziko la kum'mawa kwa Yordano

1 Ndipo Yoswa anakalamba, wa zaka zambiri; ndipo Yehova ananena naye, Wakalamba, wa zaka zambiri, ndipo latsala dziko lalikurukuru, alilandire colowa cao,

2 Dziko lotsala ndilo: malire onse a Afilisti, ndi Agesuri onse,

3 kuyambira Sihoro wokhala cakuno ca Aigupto mpaka malire a Ekironu kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asekelo, a ku Giti, ndi a ku Ekiro, ndi Ahivi;

4 kumwela dziko lonse la Akanani, ndi Meara ndiwo wa Asidoni, mpaka ku Afeka, mpaka ku malire a Aaroori;

5 ndi dziko la Agebili, ndi Lebano lonse kum'mawa, kuyambira Baala-gadi pa tsinde la phiri la Herimoni, mpaka polowera pace pa Hamati;

6 nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebano, mpaka Misirepotumaimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israyeli, koma limeneli uwagawire Aisrayeli, likhale colowa cao, monga ndinakulamulira.

7 Ndipo tsopano uwagawire mapfuko asanu ndi anai, ndi pfuko la Manase logawika pakati, dziko ili likhale colowa cao.

8 Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira colowa cao, cimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordano kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;

9 kuyambira pa Aroeri, wokhala m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi mudzi uti pakati pa cigwa, ndi cidikha conse ca Medeba mpaka ku Diboni;

10 ndi midzi yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori, wakucita ufumu m'Hesiboni, mpaka malire a ana a Amoni;

11 ndi Gileadi, ndi malire a Agesuri, ndi Amaakati, ndi phiri lonse la Herimoni, ndi Basana ionse mpaka ku Saleka;

12 ufumu wonse wa Ogi m'Basana, wakucita ufumu m'Asitarotu, ndi m'Edrei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefai); pakuti Mose anakantha awa, nawainga.

13 Koma ana a Israyeli sanainga Agesuri kapena Amaakati; koma Gesuri, ndi Maakati amakhala pakati pa Israyeli, mpaka lero lino.

14 Koma pfuko la Levi sanalipatsa colowa; nsembe za Yehova Mulungu wa Israyeli, zocitika ndi moto, ndizo colowa cace, monga iye adanena naye.

15 Ndipo Mose anapatsira pfuko la ana a Rubeni monga mwa mabanja ao.

16 Malire ao anayambira ku Aroeri wokhala m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi mudzi uli pakati pa cigwa ndi cidikha conse ca ku Medeba;

17 Hesiboni ndi midzi yace yonse yokhala pacidikha; Diboni, ndi Bamoto-baala ndi Betibaala-Meoni;

18 ndi Yahaza ndi Kedemotu, ndi Mefaata;

19 ndi Kinyataimu, ndi Sibima, ndi Zeretisahara, m'phiri la kucigwa;

20 ndi Beti-peori, ndi matsikiro a Pisiga, ndi Beti-yesimotu;

21 ndi midzi yonse ya kucidikha, ndi ufumu wonse wa Sihoni mfumu ya Aamori, wocita ufumu m'Hesiboni, amene Mose anamkantha pamodzi ndi akalonga a Midyani, Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri ndi Reba, akalonga a Sihoni, nzika za m'dziko.

22 Ana a Israyeli anaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori, mlauli uja, pamodzi ndi ena adawaphawo.

23 Ndipo malire a ana a Rubeni ndiwo Yordano ndi malire ace. Ndico colandira ca ana a Rubeni monga mwa mabanja ao, midzi yace ndi miraga yace.

24 Ndipo Mose anapatsira pfuko la Gadi, ana a Gadi, monga mwa mabanja ao.

25 Ndipo malire ao ndiwo Yazeri, ndi midzi yonse ya Gileadi, ndi dziko la ana a Amoni logawika pakati, mpaka ku Aroeri, wokhala cakuno ca Raba;

26 ndi kuyambira Hesiboni mpaka Ramati-Mizipe, ndi Betonimu; ndi kuyambira Mahanaimu mpaka malire a Dibiri;

27 ndipo m'cigwa Betiharamu, ndi Beti-nimra, ndi Sukoti, ndi Zafoni, cotsala ca ufumu wa Sihoni mfumu ya Hesiboni, Yoidano ndi malire ace, mpaka malekezero a nyanja ya Kinereti, tsidya lija la Yordano kum'mawa.

28 Ici ndi colowa ca ana a Gadi, monga mwa mabanja ao, midzi yace ndi miraga yace.

29 Mose anaperekanso colowa kwa pfuko la Manase logawika pakati, ndico ca pfuko la Manase logawika pakati monga mwa mabanja ao.

30 Ndipo malire ao anayambira ku Mahanaimu, Basana lonse, ufumu wonse wa Ogi mfumu ya ku Basana, ndi midzi yonse ya Yairi, yokhala m'Basana, midzi makumi asanu ndi limodzi;

31 ndi Gileadi logawika pakati, ndi Asitarotu ndi Edrei, midzi ya ufumu wa Ogi m'Basana, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.

32 Izi ndi zolowazi Mose anazigawira m'zidikha za Moabu, tsidya ilo la Yordano ku Yeriko, kum'mawa.

33 Koma pfuko la Levi, Mose analibe kulipatsa colowa: Yehova Mulungu wa lsrayeli, ndiye colowa cao, monga ananena nao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24