Yoswa 17 BL92

Malire a Manase

1 Gawo la pfuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Gileadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Gileadi ndi Basana.

2 Ndipo maere anagwera ana ena otsala a Manase monga mwa mabanja ao; ana a Abiezere ndi ana a Heleki, ndi ana a Asiriyeli, ndi ana a Sekemu ndi ana a Hefere, ndi ana a Semida; awa ndi ana amuna a Manase mwana wa Yosefe, monga mwa mabanja ao.

3 Koma Tselofekadi, mwana wa Hefere, mwana wa Gileadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana amuna koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana ace akazi ndiwo: Mala, ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

4 Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazare wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse colowa pakati pa abale athu; cifukwa cace anawapatsa monga mwa lamulo La Yehova, colowa pakati pa abale a atate wao.

5 Ndipo anamgwera Manase magawo khumi, osawerenga dziko la Gileadi ndi Basana lokhala tsidya lija la Yordano:

6 popeza ana akazi a Manase adalandira colowa pakati pa ana ace amuna; ndi dziko la Gileadi linakhala la ana a Manase otsala.

7 Ndipo malire a Manase anayambira ku Aseri, kumka ku Mika-metatu, wokhala cakuno ca Sekemu; namuka malire ku dzanja lamanja kwa nzika za Enitapua.

8 Dziko la Tapua linali la Manase; koma Tapua mpaka malire a Manase linakhala la ana a Efraimu.

9 Natsikira malire ku mtsinje wa Kana, kumwera kwa mtsinje; midzi iyi inakhala ya Efraimu pakati pa midzi ya Manase; ndi malire a Manase anali kumpoto kwa mtsinje; ndimaturukiro ace anali kunyanja;

10 kumwera nkwa Efraimu ndi kumpoto nkwa Manase, ndi malire ace ndi nyanja; ndi kumpoto anakomana ndi Aseri, ndi kum'mawa anakomana ndi Isakara.

11 Ndipo m'Isakara ndi m'Aseri Manase anali nao Betiseani ndi midzi yace, ndi Ibleamu ndi midzi yace, ndi nzika za Doro ndi midzi yace, ndi nzika za Eni-doro ndi midzi yace, ndi nzika za Taanaki ndi midzi yace, ndi nzika za Megido ndi midzi yace; dziko la mapiri atatu.

12 Koma ana a Manase sanatha kuingitsa a m'midzi aja, popeza Akananjanafuna kukhala m'dziko lija.

13 Ndipo kunali pamene ana a lsrayeli atakula mphamvu anasonkhetsa Akanani osawaingitsa onse.

14 Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji colowa cathu camaere cimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe?

15 Ndipo Yoswa ananena nao, Ngati muli anthu aunyinji, kwerani kuli mitengoko, ndi kudziswera minda m'dziko la Aperizi ndi la Arefai; akakuceperani malo ku phiri la Efraimu.

16 Ndipo ana a Yosefe anati, Kuphiriko sikudzatifikira; ndipo Akananionse akukhala m'dziko la cigwa ali nao magareta acitsulo, iwo akukhala m'Bete-Seani, ndi midzi yace ndi iwo omwe akukhala m'cigwa ca Yezereli.

17 Ndipo Yoswa ananena kwa iwo a m'nyumba ya Yosefe, kwa Efraimu ndi Manase, ndi kuti, Inu ndinu anthu aunyinji, muli nayo mphamvu yaikuru; simudzakhala nalo gawo limodzi lokha;

18 koma kuphiriko kudzakhala kwanu pakuti pangakhale mpa mitengo, mudzisweretu minda, ndi maturukiro ace adzakhala anu; pakuti mudzaingitsa Akanani angakhale ali nao magareta acitsulo, angakhale ali amphamvu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24